6. Ndipo iye anamuika m'cigwa m'dziko la Moabu popenyana ndi Beti-peori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwace kufikira lero lino.
7. Ndipo zaka zace za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lace silinacita mdima, ndi mphamvu yace siidaleka.
8. Ndipo ana a Israyeli analira Mose m'zidikha za Moabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose.
9. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ace; ndi ana a Israyeli anamvera iye, nacita monga Yehova adauza Mose.