Deuteronomo 34:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Moabu, monga mwa mau a Yehova.

6. Ndipo iye anamuika m'cigwa m'dziko la Moabu popenyana ndi Beti-peori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwace kufikira lero lino.

7. Ndipo zaka zace za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lace silinacita mdima, ndi mphamvu yace siidaleka.

8. Ndipo ana a Israyeli analira Mose m'zidikha za Moabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose.

9. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ace; ndi ana a Israyeli anamvera iye, nacita monga Yehova adauza Mose.

10. Ndipo sanaukanso mnereri m'lsrayeli ngati Mose, amene Yehova anadziwana naye popenyana maso;

11. kunena za zizindikilo ndi zozizwa zonse zimene Yehova anamtumiza kuzicita m'dziko la Aigupto kwa Farao, ndi anyamata ace onse, ndi dziko lace lonse;

12. ndi kunena za dzanja la mphamvu lonse, ndi coopsa cacikuru conse, cimene Mose anacita pamaso pa Israyeli wonse.

Deuteronomo 34