24. Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m'mwamba kapena pa dziko lapansi wakucita monga mwa nchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu?
25. Ndioloketu, ndilione dziko lokomali liri tsidya la Yordano, mapiri okoma aja, ndi Lebano.
26. Koma Yehova anakwiya ndi ine, cifukwa ca inu, sanandimvera ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Cikukwanire, usaonjezenso kunena ndi Ine za cinthuci.