45. Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ace ndi malemba ace amene anakulamulirani;
46. ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati cizindikilo ndi cozizwa, nthawi zonse.
47. Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi cimwemwe ndi mokondwera mtima, cifukwa ca kucuruka zinthu zonse;
48. cifukwa cace mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lacitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.
49. Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wocokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao;
50. mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamcitira cifundo mwana;