Deuteronomo 28:44-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

44. Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mcira.

45. Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ace ndi malemba ace amene anakulamulirani;

46. ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati cizindikilo ndi cozizwa, nthawi zonse.

47. Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi cimwemwe ndi mokondwera mtima, cifukwa ca kucuruka zinthu zonse;

48. cifukwa cace mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lacitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.

49. Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wocokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao;

50. mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamcitira cifundo mwana;

51. ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.

Deuteronomo 28