7. Pamenepo tinapfuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi nchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu;
8. ndipo Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukuru, ndi zizindikilo, ndi zodabwiza;
9. ndipo anabwera nafe kumalo kuno, natipatsa dziko ili ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.
10. Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kugwadira Yehova Mulungu wanu;
11. ndipo mukondwere nazo zokoma zonse zimene Yehova Mulungu wanu akupatsani, inu ndi nyumba zanu, inu ndi Mlevi, ndi mlendo ali pakati panu.