1. Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa.
2. Ndipo kudzali, wocita coipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pace, amwerengere zofikira coipa cace.
3. Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu.
4. Musamapunamiza ng'ombe popuntha tirigu.