Deuteronomo 22:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Mukacipeza cisa ca mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi mace alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga mace pamodzi ndi ana;

7. muloletu mace amuke, koma mudzitengere ana; kuti cikukomereni, ndi kuti masiku anu acuruke.

8. Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lace, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.

9. Musamabzala mbeu zosiyana m'munda wanu wamphesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wamphesa zomwe.

Deuteronomo 22