Deuteronomo 21:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. ndipo kudzali kuti mudzi wakukhala kufupi kwa munthu wophedwayo, inde akuru a mudzi uwu atenge ng'ombe yamsoti yosagwira nchito, yosakoka goli;

4. ndipo akuru a mudzi uwu atsike nao msotiwo ku cigwa coyendako madzi, cosalima ndi cosabzala, naudula khosi msotiwo m'cigwamo;

5. ndipo ansembe, ana a Levi, ayandikize; pakuti Yehova Mulungu wanu anasankha iwo kumtumikira ndi kudalitsa m'dzina la Yehova; ndipo kutengana konse ndi kupandana konse kukonzeke monga mwa mau awa.

6. Ndipo akuru onse a mudziwo wokhala pafupi pa munthu wophedwayo azisamba manja ao pa msoti woudula khosi m'cigwamo;

7. nayankhe nati, Manja athu sanakhetsa mwazi uwu, ndi maso athu sanauona.

8. Landirani, Yehova, cotetezera anthu anu Israyeli, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosacimwa ukhale pakati pa anthu anu Israyeli; ndipo adzawatetezera ca mwaziwo.

9. Cotero mudzicotsere mwazi wosacimwa pakati panu, pakuti wacita coyenera pamaso pa Yehova.

Deuteronomo 21