Deuteronomo 15:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Muzidye caka ndi caka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene Yehova adzasankha, inu ndi a m'banja mwanu.

21. Koma ikakhala naco cirema, yotsimphina, kapena yakhungu, cirema ciri conse coipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.

22. Muidye m'mudzi mwanu; odetsa ndi oyera aidye cimodzimodzi, monga mphoyo ndi nswala.

23. Mwazi wace wokha musamadya; muuthire pansi ngati madzi.

Deuteronomo 15