Deuteronomo 15:15-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo mukumbukile kuti munali akapolo m'dziko la Aigupto, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; cifukwa cace ndikuuzani ici lero lino.

16. Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituruka kucoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu;

17. pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwace, kulikanikiza ndi citseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzicitanso momwemo ndi adzakazi anu.

18. Musamayesa neosautsa, pomlola akucokereni waufulu; popeza anakugwirirani nchito zaka zisanu ndi cimodzi monga wolipidwa wakulandira cowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzicita.

Deuteronomo 15