Deuteronomo 14:23-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo muzidye pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo m'mene asankhamo iye, kukhalitsamo dzina lace; limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, la vinyo wanu, ndi la mafuta anu, ndi oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi a nkhosa ndi mbuzi zanu; kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.

24. Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simukhoza kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lace, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu;

25. pamenepo mulisinthe ndarama, ndi kumanga ndarama ikhale m'dzanja mwanu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;

26. ndipo mugule ndi ndaramazo ciri conse moyo wanu ukhumba, ng'ombe kapena nkhosa, kapena vinyo, kapena cakumwa colimba, kapena ciri conse moyo wanu ukufunsani; nimudye pomwepo pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera, inu ndi a pabanja panu.

27. Koma Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu.

28. Pakutha pace pa zaka zitatu muziturutsa magawo onse a magawo khumi a zipatso zanu za caka ico, ndi kuwalinditsa m'mudzi mwanu;

29. ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu nchito zonse za dzanja lanu muzicitazi.

Deuteronomo 14