29. Pamene Yehova Mulungu wanu akadzadulatu amitundu pamaso panu, kumene mulowako kuwalandira, ndipo mutawalandira, ndi kukhala m'dziko lao,
30. dzicenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yao, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yao bwanji? ndicite momwemo inenso.
31. Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti ziri zonse zinyansira Yehova, zimene azida iye, iwowa anazicitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao amuna ndi ana ao akazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.
32. Ciri conse ndikuuzani, mucisamalire kucicita; musamaoniezako, kapena kucepsako.