22. Koma monga umo amadya mphoyo ndi ngondo momwemo uzizidya; odetsa ndi oyera adyeko cimodzimodzi.
23. Koma mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yace.
24. Musamadya uwu; muuthire pansi ngati madzi.
25. Musamadya uwu; kuti cikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu, pakucita inu zoyenera pamaso pa Yehova.