Danieli 5:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pamenepo padasandulika pa nkhope pace pa mfumu, ndi maganizo ace anamsautsa, ndi mfundo za m'cuuno mwace zinaguruka, ndi maondo ace anaombana.

7. Nipfuulitsa mfumu abwere nao openda, Akasidi, ndi alauli, Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babulo, Ali yense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwace, adzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwace, nadzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwu.

8. Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoza kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwace.

9. Ndipo mfumu Belisazara anabvutika kwambiri, ndi nkhope yace inasandulika, ndi akuru ace anathedwa nzeru.

Danieli 5