6. Cifukwa cace ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babulo, kuti andidziwitse kumasulira kwace kwa lotoli.
7. Pamenepo anafika alembi, openda, Akasidi, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitsa kumasulira kwace.
8. Koma potsiriza pace analowa pamaso panga Danieli, dzina lace ndiye Belitsazara, monga mwa dzina la mulungu wanga, amenenso muli mzimu wa milungu yoyera m'mtima mwace; ndipo ndinamfotokozera lotoli pamaso pace, ndi kuti,