26. Ndipo kuti anauza asiye citsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira.
27. Cifukwa cace, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani macimo anu ndi kucita cilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kucitira aumphawi cifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.
28. Conseci cinagwera mfumu Nebukadinezara.
29. Itatha miyezi khumi ndi iwiri, analikuyenda m'cinyumba cacifumu ca ku Babulo.
30. Mfumu inanena, niti, Suyu Babulo wamkuru ndinammanga, akhale pokhala pacifumu, ndi mphamvu yanga yaikuru uoneke ulemerero wa cifumu canga?
31. Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ocokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakucokera.