19. Pamenepo cinsinsico cinabvumbulutsidwa kwa Danieli m'masomphenya a usiku. Ndipo Danieli analemekeza Mulungu wa Kumwamba.
20. Danieli anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi, a pakuti nzeru ndi mphamvu ziri zace;
21. pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, acotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi cidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.
22. Iye abvumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.
23. Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ici tacifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.