Danieli 1:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Nati mkuru wa adindo kwa Danieli. Ine ndiopa mbuyanga mfumu, amene anakuikirani cakudya canu ndi cakumwa canu; pakuti aonerenji nkhope zanu zacisoni zoposa za anyamata olingana ndi inu? momwemo mudzaparamulitsa mutu wanga kwa mfumu.

11. Nati Danieli kwa kapitao, amene mkuru wa adindo adamuikayo ayang'anire Danieli, Hananiya, Misaeli, ndi Azariya,

12. Muyesetu anyamata anu masiku khumi; atipatse zomera m'nthaka tidye, ndi madzi timwe.

13. Pamenepo mupenye maonekedwe athu ndi maonekedwe a anyamata akudya cakudya ca mfumu; ndi monga umo muonera, mucitire anyamata anu.

14. Ndipo anawamvera mau awa, nawayesa masiku khumi.

15. Atatha masiku khumiwo tsono, anaona kuti maonekedwe ao ndi kunenepa kwao anaposa anyamata onse adadyawo zakudya za mfumu.

16. Pamenepo kapitaoyo anacotsa cakudya cao ndi vinyo akadamwa, nawapatsa zomera m'nthaka.

17. Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa cidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Danieli anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.

18. Atatha masiku inanenawo mfumu kuti alowe nao, mkulu wa adindo analowa nao pamaso pa Nebukadinezara.

Danieli 1