6. ndipo ku mpandowo, ngati nyanja, yamandala yonga krustalo; ndipopakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzaia ndi maso kutsogolo indi kumbuyo.
7. Ndipo camoyo coyamba cinafanana nao mkango, ndi camoyo caciwiri cinafanana ndi mwana wa ng'ombe, ndi camoyo cacitatu cinali nayo nkhope yace ngati ya munthu, ndi camoyo cacinai cidafanana ndi ciombankhanga cakuuluka.
8. Ndipo zamoyozo zinai, conse pa cokha cinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.
9. Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa iye wakukhala pa mpando wacifumu, kwa iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi,