Cibvumbulutso 21:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. ndipo adzawapukutira misozi yonse kuicotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena cowawitsa; zoyambazo zapita.

5. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wacifumu anati, Taonani, ndicita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona.

6. Ndipo anati kwa ine, Zatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza. Kwa iye wakumva ludzu ndidzampatsa amwe ku kasupe wa madzi a moyo kwaulere.

7. Iye wakulakika adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wace, ndi iye adzakhala mwana wanga.

8. Koma amantha, ndi osakhulupira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi acigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, colandira cao cidzakhala m'nyanja yotentha ndi mota ndi sulfure; ndiyo imfa yaciwiri.

Cibvumbulutso 21