25. Koma 5 cimene muli naco, gwirani kufikira ndikadza.
26. Ndipo iye amene alakika, ndi iye amene asunga nchito zanga kufikira citsiriziro, kwa iye 6 ndidzapatsa ulamuliro wa pa amitundu;
27. ndipo 7 adzawalamulira ndi ndodo yacitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga lnenso ndalandira kwa Atate wanga;
28. ndipo ndidzampatsa iye 8 nthanda.
29. Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.