Cibvumbulutso 2:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba;Izi azinena iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lace lamanja, iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi:

2. Ndidziwa nchito zako, ndi cilemetso cako ndi cipiriro cako, ndi kuti sukhoza kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzicha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;

3. ndipo uli naco cipiriro, ndipo walola cifukwa ca dzina langa, wosalema.

4. Koma ndiri nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya cikondi cako coyamba.

5. Potero kumbukila kumene wagwerako, nulape, nucite nchito zoyamba; koma ngari sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa coikapo nyali cako, kucicotsa pamalo pace, ngati sulapa.

Cibvumbulutso 2