Cibvumbulutso 19:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikuru, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, nizinena, Aleluya; pakuti acita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.

7. Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wace wadzikonzera.

8. Ndipo anampatsa iye abvale bafuta wonyezimira woti mbu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.

9. Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.

10. Ndipo ndinagwa pa mapazi ace kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa cinenero.

Cibvumbulutso 19