3. Cifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa cigololo cace mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anacita naye cigololo; ndipo ocita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyererakwace.
4. Ndipo ndinamva mau ena ocokera Kumwamba, nanena, Turukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi macimo ace, ndi kuti mungalandireko ya miliri yace;
5. pakuti macimo ace anaunjikizana kufikira m'Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zace.
6. Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa nchito zace; m'cikhomo unathiramo, muuthirire cowirikiza.
7. Monga momwe unadzicitira ulemu, nudyerera, momwemo muucitire eouzunza ndi couliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwace, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.
8. Cifukwa cace miliri yace idzadzam'tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; cifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.
9. Ndipo mafumu a dziko ocita cigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwace, poima patali,