Cibvumbulutso 18:23-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. 1 ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m'dziko; pakuti 2 ndi nyanga yako mitunduyonse inasokeretsedwa.

24. Ndipo 3 momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.

Cibvumbulutso 18