Cibvumbulutso 18:11-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo ocita malonda a m'dziko adzalira nadzaucitira cifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;

12. malonda a golidi, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wace, ndi a ngale, ndi a nsaru yabafuta, ndi a cibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya pfungo lokoma, ndi cotengera ciri conse ca minyanga ya njobvu, ndi cotengera ciri conse camtengo wa mtengo wace wapatali, ndi camkuwa ndi cacitsulo, ndi cansangalabwi;

13. ndi kinamomo ndi amomo, ndi zofukiza, ndi zodzola, ndi libano, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magareta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.

14. Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakucokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.

Cibvumbulutso 18