Cibvumbulutso 14:7-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. ndi kunena ndi mau akuru, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya ciweruziro cace; ndipo mlambireni iye amene analenga m'mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi,

8. Ndipo anatsata mngelo wina mnzace ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babulo waukuru umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa cigololo cace.

9. Ndipo anawatsata mngelo wina, wacitatu, nanena ndi mau akuru, Ngati wina alambira ciromboco, ndi fane lace, nalandira lembapamphumi pace, kapena pa dzanja lace,

Cibvumbulutso 14