5. ndi kwa Yesu Kristu, mboli yokhulupirikayo, wobadwa woyanba wa akufa, ndi mkulu wa mafunu a dziko lapansi, Kwa iye ameieatikonda ife, natimasula ku macimo athu ndi mwazi wace;
6. natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wace; kwa iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.
7. Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a pa dziko adzamlira iye. Terotu. Amen.
8. Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.