Cibvumbulutso 1:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a cineneroco, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.

4. Yohane kwa Mipingo isanu ndi wiri m'Asiya: Cisomo kwa inu ndi ntendere, zocokerakwa iye amene ili, ndi amene adali, ndi amene aliikudza; ndi kwa mizimu isanu ndi wiri yokhala ku mpando wacifumu vace;

5. ndi kwa Yesu Kristu, mboli yokhulupirikayo, wobadwa woyanba wa akufa, ndi mkulu wa mafunu a dziko lapansi, Kwa iye ameieatikonda ife, natimasula ku macimo athu ndi mwazi wace;

6. natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wace; kwa iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.

7. Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a pa dziko adzamlira iye. Terotu. Amen.

8. Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.

Cibvumbulutso 1