Aroma 8:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za thupi, mudzakhala ndi moyo.

14. Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu,

15. Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,

16. Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu;

17. ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.

18. Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.

19. Pakuti ciyembekezetso ca colengedwa cilimilia bvumbulutso la ana a Molungu.

Aroma 8