20. wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'cilamulo ndi cionekedwe ca nzeru ndi ca coonadi;
21. ndiwe tsono wakuphunzitsa wina; kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?
22. Iwe wakunena kuti munthu asacite cigololo, kodi umacita cigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za m'kacisi kodi?
23. Iwe wakudzitamandira pacilamulo, kodi ucitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'cilamulo?