Aroma 16:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. amene anapereka khosi lao cifukwa ca moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu;

5. ndipo mulankhule Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Mulankhule Epeneto wokondedwa wanga, ndiye cipatso coundukula ca Asiya ca kwa Kristu,

6. Mulankhule Mariya amene anadzilemetsa ndi nchito zambiri zothandiza inu.

7. Mulankhule Androniko ndi Yuniya, anansi anga, ndi andende anzanga, amene ali omveka mwa amitumwi, amenenso ananditsogolera ine mwa Kristu.

Aroma 16