10. Ndiponso anena,Kondwani, amitundu inu, pamodzindi anthu ace.
11. Ndiponso,Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse;Ndipo anthu onse amtamande.
12. Ndiponso, Yesaya ati,Padzali muzu wa Jese,Ndi iye amene aukira kucita ufumu pa anthu amitundu;Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.
13. Ndipo Mulungu wa ciyembekezo adzaze inu ndi cimwemwe conse ndi mtendere m'kukhulupira, kuti mukacuruke ndi ciyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
14. Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzace.