Aroma 13:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuti ili, Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina liri lonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.

10. Cikondano sicicitira mnzace coipa; cotero cikondanoco ciri cokwanitsa lao mulo.

11. Ndipo citani ici, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano cipulumutso cathu ciri pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupira.

12. Usiku wapita, ndi dzuwa layandikira; cifukwa cace tibvule nchito za mdima, ntibvale camuna ca kuunika.

13. Tiyendeyeode koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'cigololo ndi conyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.

Aroma 13