Aroma 13:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Cifukwa cace, kuyenera kuti mukhale omvera, si cifukwa ca mkwiyo woo kha, komanso cifukwa ca cikumbu mtima.

6. Pakuti cifukwa ca ici mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndi wo atumiki a Mulungu akulabadira be cinthu cimeneci.

7. Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ace a msonkho; kuli pira kwa eni ace a kulipidwa; kuopa kwa eni ace a kuwaopa; ulemu kwe eni ace a ulemu.

8. Musakhale ndi mangawa kwa munthu ali yense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzace wakwanitsa lamulo.

9. Pakuti ili, Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina liri lonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.

Aroma 13