Aroma 12:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa cisomo copatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa cikhulupiriro;

7. kapenayakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako;

8. kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira acite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi cangu; iye wakucita cifundo, acite ndi kukondwa mtima.

9. Cikondano cikhale copanda cinyengo, Dana naco coipa; gwirizana naco cabwino.

10. M'cikondano ca anzanu wina ndi mnzace mukondane ndi cikondi ceni ceni; mutsogolerane ndi kucitira wina mnzace ulemu;

11. musakhale aulesi m'macitidwe anu; khalani acangu mumzimu, tumikirani Ambuye;

12. kondwerani m'ciyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani cilimbikire m'kupemphera,

13. Patsani zosowa oyera mtima; cerezani aulendo.

Aroma 12