6. Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa cisomo copatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa cikhulupiriro;
7. kapenayakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako;
8. kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira acite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi cangu; iye wakucita cifundo, acite ndi kukondwa mtima.
9. Cikondano cikhale copanda cinyengo, Dana naco coipa; gwirizana naco cabwino.
10. M'cikondano ca anzanu wina ndi mnzace mukondane ndi cikondi ceni ceni; mutsogolerane ndi kucitira wina mnzace ulemu;
11. musakhale aulesi m'macitidwe anu; khalani acangu mumzimu, tumikirani Ambuye;