Aroma 12:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. comweco ife, ndife ambiri, tiri thupi limodzi mwa Kristu, ndi ziwalo zinzace, wina ndi wina.

6. Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa cisomo copatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa cikhulupiriro;

7. kapenayakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako;

8. kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira acite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi cangu; iye wakucita cifundo, acite ndi kukondwa mtima.

9. Cikondano cikhale copanda cinyengo, Dana naco coipa; gwirizana naco cabwino.

Aroma 12