1. Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.
2. Pakuti ndiwacitira iwo umboni kuti a ali ndi cangu ca kwa Mulungu, koma si monga mwa cidziwitso.
3. Pakuti pakusadziwa cilungamo ca Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa cilungamo ca iwo okha, iwo sanagonja ku cilungamo ca Mulungu.