Amosi 8:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Koma nyimbo za kukacisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzacuruka; adzaitaya pali ponse padzakhala zii.

4. Tamverani ici, inu akumeza aumphawi, ndi kuwatha ofatsa m'dziko, ndi kuti,

5. Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? ndi kucepsa efa, ndi kukuliitsa sekeli, ndi kucenjerera nayo miyeso yonyenga;

6. kuti tigule osauka ndi ndarama, ndi aumphawi ndi nsapato, ndi kugulitsa nsadwa za tirigu.

7. Yehova walumbira pali kudzikuza kwa Yakobo, Ngati ndidzaiwala konse nchito zao ziri zonse?

8. Kodi dziko silidzanjenjemera cifukwa ca ici, ndi kulira ali yense wokhalamo? inde lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; lidzagwedezeka, ndi kutsikanso ngati mtsinje wa Aigupto,

Amosi 8