Amosi 7:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. ndi misanje ya Isake idzakhala bwinja; ndi malo opatulika a Israyeli adzapasuka; ndipo ndidzaukira nyumba ya Yerobiamu ndi lupanga.

10. Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza kwa Yerobiamu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Amosi wapangira inu ciwembu pakati pa nyumba ya Israyeli; dziko silikhoza kulola mau ace onse.

11. Pakuti atero Amosi, Yerobiamu adzafa ndi lupanga, ndi Israyeli adzatengedwadi ndende, kucoka m'dziko lace.

Amosi 7