Amosi 7:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. koma usaneneranso ku Beteli; pakuti pamenepo mpa malo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yacifumu.

14. Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakuchera nkhuyu;

15. ndipo Yehova ananditenga ndirikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israyeli.

16. Cifukwa cace tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera cotsutsana ndi Israyeli, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isake;

Amosi 7