2. Pitani ku Kaline, nimuone; kucokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? kapena malire ao aposa malire anu?
3. Inu akutalikitsa tsiku loipa, ndi kusendeza pafupi mpando waciwawa;
4. ogona pa makama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya ana a nkhosa a ku zoweta, ndi ana a ng'ombe ocoka pakati pa khola;
5. akungoyimba kutsata maliridwe a zeze, nadzilingiririra zoyimbira nazo Ingati Davide;
6. akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa cisoni ndi kutyoka kwa Yosefe.
7. Cifukwa cace tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.