Amosi 5:13-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Cifukwa cace wocenierayo akhala cete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.

14. Funani cokoma, si coipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wamakamu adzakhala ndi inu, monga munena.

15. Danani naco coipa, nimukonde cokoma; nimukhazikitse ciweruzo kucipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzacitira cifundo otsala a Yosefe.

16. Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! kalanga ine! nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire.

17. Ndi m'minda yonse yamipesa mudzakhala kulira, pakuti ndipita pakati pako, ati Yehova.

18. Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova! mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? ndilo mdima, si kuunika ai.

19. Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi cimbalangondo cikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lace, nimluma njoka.

20. Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo?

Amosi 5