14. Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yace, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wace;
15. ndi wokoka uta sadzalimbika, ndi waliwiro sadzadzipulumutsa; ngakhale woyenda pa akavalo sadzapulumutsa moyo wace;
16. ndi wolimba mtima mwa ngwazi adzathawa wamarisece tsiku lomwelo, ati Yehova.