6. Mau anu akhale m'cisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akarani.
7. Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tukiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:
8. amene ndamtuma kwa inu cifukwa ca ici comwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu;
9. pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu.