4. kuti ndicionetse ici monga ndiyenera kulankhula.
5. Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kucita macawi nthawi ingatayike.
6. Mau anu akhale m'cisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akarani.
7. Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tukiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:
8. amene ndamtuma kwa inu cifukwa ca ici comwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu;