Akolose 4:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pakuti ndimcitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo nchito cifukwa ca inu, ndi iwo a m'Laodikaya, ndi iwo a m'Herapoli.

14. Akulankhulani inu Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema.

15. Lankhulani abalewo a m'Laodikaya, ndi Numfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao.

16. Ndipo pamene mudamwerenga kalata uyu, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikaya, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikaya,

Akolose 4