12. Akulankhulani inu Epafra ndiye wa kwa inu ndiye kapolo wa Yesu Kristu, wakulimbira cifukwa ca inu m'mapemphero ace znasiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'cifuniro conse ca Mulungu.
13. Pakuti ndimcitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo nchito cifukwa ca inu, ndi iwo a m'Laodikaya, ndi iwo a m'Herapoli.
14. Akulankhulani inu Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema.
15. Lankhulani abalewo a m'Laodikaya, ndi Numfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao.